Mipingo ikumana ndi boma pa ngongole za dziko lino

Gama: TIli ndi udindo okumana ndi boma
Bungwe la mipingo ya chikhirisitu la Malawi Council of Churches lati likhale likukumana ndi akuluakulu aboma kuti akambirane za ngongole yokwana K15 trillion yomwe dziko lino lilinayo.
Ngongoleyi yakwera ndi K2.5 Trillion ndipo yafika pa K15.1 Trilion chaka chino kuchoka pa K13 Trllion chaka chatha.
Malingana ndi wapampando wa bungweli Billy Gama, mipingo ili ndi mphavu zoyankhulira amalawi omwe sangakwanitse kufikira adindo pa nkhani zosiyanasiya zokhudza dziko lino kuphatikizapo zachuma.
Iye wati ngati bungwe ali ndi chidwi chofuna kudziwa kuti ngongolezi zinagwira ntchito yanji komanso kuti boma laika ndondomeko zotani zobwezera ngongolezi popanda kubweretsa mavuto ena pakati pa amalawi omwe ambiri akukumana kale ndi Mavuto ankhaninkhani.
‘’Ngati Mipingo tili ndi udindo waukulu othandiza anthu kuti nkhawa zawo zifike kwa adindo omwe anapatsidwa mphavu yoyendetsa boma mmalo mwawo.
‘’Adindo ali ndi udindo waukulu owuza anthu tsatanetsatane wawomwe zinthu zosiyanasiyana zikuyendera popanda kufunzidwa kapena kukakamizidwa,’’ watero Gama.
Koma ngakhale izi zili chomwechi, Gama wati bungwe lake likukambirana kaye ndi magulu ena okhudzidwa kuti akhale ndi liwu limodzi lamphanvu lokawafikila akuluakulu abomawa.
Pakadali pano, iye sanafotokoze zambiri za magulu omwe akhale akukumana nawo kuti akambirane za nkhaniyi komanso kuti akuluakulu abomawa afikiridwa liti komanso munjira yanji.