Mr Jokes waselewula ndiwo za gulu
![](https://i0.wp.com/www.capitalradiomalawi.com/wp-content/uploads/2024/08/Jokes-and-soya-pieces.jpeg?fit=960%2C469&ssl=1)
Wachitira nthabwala ndiwo -Mr Jokes
Pamene chiwelengero cha anthu ochuluka chikumadya ndiwo za soya pieces mdziko muno kaamba ka chikondi, kuchepekedwa ngakhalenso kutsatira kusachedwa kupsa kwa ndiwozi, katswiri wochita nthabwala, Mr Jokes, waseleula kampani zopanga ndiwozi.
Mukukamba kwake, Mr Jokes waonetsa kuti ndiwozi amazidziwa bwino lomwe moti mpaka anafika poloweza kachulukidwe kake mu paketi iliyonse ngakhale sanatsindike pa nambala yeniyeni ya nthuli zomwe iye amayembekezera kuti zidzipezekamozo.
Polemba pa tsamba lake la mchezo pa Facebook, katswiriyu wati: “Komatu ofunika Ma company opanga soya pieces wa azitolere, Nanga pena akumapezekamo 48, pena 36, pena 52, pena 41, pena 29, zikukhala Bwanji Kweni Kweni?”
Ophunzira msukulu zaukachenjede omwe samagonera pa sukulu zawozo (self-boarders) ndi ena mwa omwe ndiozinso amazidya koma tsamba lino silikukhulupilira kuti alipo analoweza za nthulizo.