Maanja oposa 100 sauzande apindula ndi ‘Mtukula Pakhomo wa M’mizinda’ – Capital Radio Malawi
15 April, 2024

Maanja oposa 100 sauzande apindula ndi ‘Mtukula Pakhomo wa M’mizinda’

Watulutsa chikalata cha uthengawu -Tchereni

Boma likuyembekezeka kupereka ndalama zokwana K15.7 billion kwa anthu omwe ali pa umphawi ndipo amakhala m’mizinda.

Izi zichitika kudzera mu ndondomeko yotchedwa ‘Mtukula Pakhomo wa M’mizinda’.

Maanja okwana oposa 100,000 a m’mizinda ya Blantyre, Lilongwe, Mzuzu ndi Zomba ndi omwe alandire ndalamazi.

 “Banja lililonse lilandira kamodzi K150,000 m’miyezi itatu ya January mpaka March chaka chino pomwe ndondomekoyi ikhale ikugwira ntchito. Maanjawa onse Pamodzi ndi 105,000,” chatero chikalata chomwe chomwe watulutsa ndi mlembi wamkulu muunduna wa za chuma Betchani Tchereni:.

Ndalamayi ikuyembekezeka kuthandiza anthuwa ku mavuto omwe dziko lino likukumana nawo makamaka kukwera mtengo kwa katundu, ngozi zogwa mwadzidzidzi komanso njala.

Ndalamazi zachokera ku thumba lotchedwa Malawi Social Protection Multi-Donor-Trust Fund kudzera ku thandizo lochokera ku World Bank, Ireland, Norway, USAID, Iceland, European Union komanso UK-FCDO .

About The Author

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *