Kauniuni akupenekera zokolola zochuluka – Capital Radio Malawi
15 April, 2024

Kauniuni akupenekera zokolola zochuluka

Lipoti likuti chimanga chitha kukololedwa chochuluka (chithunzi chotengedwa pa utatavu wa mchezo)

Gawo loyamba la kawuniwuni wa m’mene dziko lino lingachitire pa zokolola za kumunda, likuonetsa kuti dziko lino likhoza kukolola chimanga chokwana matani 3.6 miliyoni.

Mlingowu ndi okwera ndi 2.8 percent poyerekeza ndi chaka chatha pamene dziko lino lidakolola matani okwana 3.5 miliyoni.

Ndipo kawuniwuniyu akuonetsa kuti dziko lino likhoza kukolola mpunga wokwana matani 166,364 umene ndi okwera ndi 38 percent poyerekeza ndi kawuniwuni womaliza wa chaka chatha.

Malingana ndi nduna ya za ulimi Sam Kawale, fodya woposa matani 144.6 million kilograms ndiyemwe akololedwe ndipo mlingo wake omwe wakwera ndi 20.5 percent.

“Mlingo wa zokolola zambiri ukhoza kukwera poyerekeza ndi chaka chatha komabe lipoti lomaliza la m’mene dziko lino lingachitire ndi limene lifotokoze zonse. Anthu sakuyenera kuda nkhawa ndi zotsatira zakawuniwuniyu chifukwa choti lipoti lachiwiri lituluka mwezi wa mawa,” watero Kawale.

Dziko lino likuyembekezeka kukolola chinangwa, mbatana ndi nanazi zochepa

About The Author

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *