Wapolisi oganiziridwa kudzetsa kuduka dzanja kwa mwana akuyankha mulandu
Mulandu wa wapolisi yemwe akuganiziridwa kuti akukhudzidwa ndi kudulidwa dzanja komanso zara ziwiri za nyamata wa zaka 13 wayambika m’boma la Mulanje.
Mkulu ozenga milandu ya boma wayambitsa milanduyi mamabungwe ena monga a Centre for Human Rights, Education Advice and Assistance (CHREAA), Southern Africa Litigation Centre (SALC) komanso Malawi Human Rights Commission (MHRC) atayankhurapo kuti wapolisiyu azengedwe mlandu.
Omwe akuimira mwana yemwe adaduka dzanjayo ndi Chikondi Chijozi, Ruth Kaima, Brenda Khwale ndi Luntha Chimbwete.
Frackson Chigalu yemwe amagwira ntchito pa polisi ya Misanjo m’boma la Mulanje akuganiziridwa kuti anasunga nyamatayo muchitokosi kwa masiku anayi ali womangidwa ndi malamba.
Izi zinachititsa kuti madotolo adule dzanja la manja la mnyamatayo komanso zara ziwiri kudzanja la manzere kaamba koti manjawo anawonongeka kwambiri.
Mnyamatayu akuti amaganiziridwa kuti anaba ndalama za munthu wina wochita malonda.
Malipoti ena akuti mwini ndalamayo ndiyemwe adamugwira mnyamatayo ndikumumanga malamba ndipo analamula kuti asamasulidwe.
Victor Mhango yemwe ndi mkulu wa bungwe la CHREAA wauza www.capitalradiomalawi.com kuti chomwe iwo akufuna ndichoti chilungamo chidziwike.
“Makolo ake a mnyamatayu anatifikira kuti tiwathandize pankhaniyi kaamba koti nkhani zambiri zokhudza apolisi sizimayenda bwino ukakhala kuti mlandu akuyendetsa ndi apolisi anzawo,” adatero Mhango.
Anthu ena omwe athilirapo ndemanga pankhaniyi pamasamba amchezo akuti akudabwa kuti zatheka bwanji kuti wapolisi m’modzi pamasiku anayi omwe mnyamatayo anali omangidwa amagwira ntchito yekha usana ndi usiku ndiye kuti apolisi anzake sakanatha kumumasula mnyamatayo kapena wapolisi oyang’anira malowo.