Ofuna otsogoleri alonjeza kuthetsa njala, umphawi – Capital Radio Malawi
14 April, 2024

Ofuna otsogoleri alonjeza kuthetsa njala, umphawi

Akufuna kuimira utsogoleri wa dziko -Mbewe

M’modzi mwa omwe awonetsa chidwi chodzapikisana nawo pa mpando wa m’tsogoleri wa dziko lino pazisankho za 2025 David Mbewe wati msanamila ya mfundo zake yagona pothetsa umphawi komaso njala.

Mbewe yemwe posachedwapa wakhazikitsa chipani chake chotchedwa Liberation for Economic Freedom (LEF) amayankhura izi pomwe amagawa katundu osiyanasiyana yemwe ndikuphatikizapo ufa ku Machinga sabata latha.

Mbewe yemwe ndi mwini komanso m’busa wa mpingo wa Living Word Evangelistic Church wati adzaonesetsa kuti anthu adzakhale ndi chakudya chokwanira akadzavoteredwa ndikukhala m’tsogoleri wa dziko lino.

Mwazina, iye wati azaonetsetsa kuti aMalawi ambiri maka akumudzi ali ndi mwayi waukulu opeza zipangizo za ulimi pamtengo ozizira.

“Umphawi ndi njala ndizomwe zikupha aMalawi ochuluka kunjaku. Nthawi yakwana tsopano kuti ndipulumutse mtundu wanga kumavutowa. Ndili pano kulonjeza kudzathetsa umphawi, njala, nthenda ngakhale nsanje pakuti izi zikuzunza mtundu wanga,” Mbewe anatsindika.

Poyankhapo pa zomwe mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera ananena pomwe amatsekulira mkumano wa aphungu akunyumba yamalamulo owunika ndondomeko ya chuma ya chaka chino mpakana chaka cha mawa lachisanu sabata yangothayi, Mbewe wati palibe chachilendo chomwe Chakwera ananena, ponena kuti sizikusiyana ndi zomwe wakhala akunena m’mbuyomu ngakhale asanakhale m’tsogoleri wadziko lino.

“Mzoseketsa komaso zomvetsa chisoni kuti mtsogoleri alipoyu (Chakwera) akungokhala namabwereza zomwe wakhala akulonjeza kwakanthawi koma osakwaniritsa. Izi zikuwapweteka aMalawi omwe tsopano maso awo ali pa ine kuti awapulumutse,” Mbewe anafotokoza.

About The Author

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *