Ama 2 sauzande akupwetekani aMolotoni -Wikise – Capital Radio Malawi
12 September, 2024

Ama 2 sauzande akupwetekani aMolotoni -Wikise

Wachenjeza zakagwiritsidwe ntchito ka ndalama: Wikise

Oyimba wamdziko muno Wikise yemwe dzina lake lenileni ndi Frank Chawinga watulutsa nyimbo yoonera m’mawa lero ‘aMolo’ yomwe akulangiza abambo omwe akagwira ndalama sakhala pakhomo.

Nyimboyi ikuonetsa banja lamkulu wina amene wavala dzina la Molotoni likukhala muumphawi wadzaoneni, kusowa chakudya, ana kusowa zovala, komanso kutulutsidwa mnyumba, chonsecho bambo wakhomoli ali kumanyaudings.

“Abambo ambiri amatayilira akapeza ndalama ena ndalama zake zimakhalanso zangongole kupita nazo kumaphwando, kusangalala ndi akazi oyendayenda komanso kumwera mowa tsoka ilo kutengakonso matenda, ndichifukwa chake ndaganiza zoimba nyimboyi,” Watelo Wikise titayankhura naye atangotulutsa nyimboyi.

Chimodzi mwa zithunzi za kanema watsopanoyu kuonetsa aMolotoni ndi mkazi wachichepere

AMolotoni, mkanapola moto…Amolo mkanapola fire…Ama 2 sauzande akupwetekani aMolotoni…ama 2 pin akuvulazani aMolotoni…’ Ikumamveka choncho nyimboyi pena.

Kuimvetsera bwino nyimboyi ikumapereka matanthauzo awiri maka pa ndeime ili m’mwambayi yomwe ikutanthauza kuti ana obadwa mzaka zam’ma 2000 awapweteka komanso kuti akazi ogulitsa matupi awo monga ma K2,000 awapweteka.

Kanema wa nyimboyi akuonetsanso mkazi amene aMolotoni amayenda naye akunena kuti aika pa m’mbalambanda zithunzi zolaula za bamboyu ngati sakwanitsa kupereka ndalama zokwana K20,000,000 ngati chitsekapakamwa.

‘Habusa Che Wikise Baba’ monga momwe amadzitchulira mwini wake, anaimbakonso nyimbo zodziwika bwino monga Chibomba, Male, Njoyako komanso Manyau mwazina.

About The Author

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *